< اَلْمَزَامِيرُ 18 >

لِإِمَامِ ٱلْمُغَنِّينَ. لِعَبْدِ ٱلرَّبِّ دَاوُدَ ٱلَّذِي كَلَّمَ ٱلرَّبَّ بِكَلَامِ هَذَا ٱلنَّشِيدِ فِي ٱلْيَوْمِ ٱلَّذِي أَنْقَذَهُ فِيهِ ٱلرَّبُّ مِنْ أَيْدِي كُلِّ أَعْدَائِهِ وَمِنْ يَدِ شَاوُلَ. فَقَالَ: أُحِبُّكَ يَارَبُّ، يَا قُوَّتِي. ١ 1
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide mtumiki wa Yehova. Iye anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli. Davide anati: Ine ndimakukondani Inu Yehova, mphamvu zanga.
ٱلرَّبُّ صَخْرَتِي وَحِصْنِي وَمُنْقِذِي. إِلَهِي صَخْرَتِي بِهِ أَحْتَمِي. تُرْسِي وَقَرْنُ خَلَاصِي وَمَلْجَإِي. ٢ 2
Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga; Mulungu wanga ndi thanthwe langa mʼmene ndimathawiramo. Chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa, ndi linga langa.
أَدْعُو ٱلرَّبَّ ٱلْحَمِيدَ، فَأَتَخَلَّصُ مِنْ أَعْدَائِي. ٣ 3
Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando, ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.
اِكْتَنَفَتْنِي حِبَالُ ٱلْمَوْتِ، وَسُيُولُ ٱلْهَلَاكِ أَفْزَعَتْنِي. ٤ 4
Zingwe za imfa zinandizinga; mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
حِبَالُ ٱلْهَاوِيَةِ حَاقَتْ بِي. أَشْرَاكُ ٱلْمَوْتِ ٱنْتَشَبَتْ بِي. (Sheol h7585) ٥ 5
Anandimanga ndi zingwe za ku manda; misampha ya imfa inalimbana nane. (Sheol h7585)
فِي ضِيقِي دَعَوْتُ ٱلرَّبَّ، وَإِلَى إِلَهِي صَرَخْتُ، فَسَمِعَ مِنْ هَيْكَلِهِ صَوْتِي، وَصُرَاخِي قُدَّامَهُ دَخَلَ أُذُنَيْهِ. ٦ 6
Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize. Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.
فَٱرْتَجَّتِ ٱلْأَرْضُ وَٱرْتَعَشَتْ، أُسُسُ ٱلْجِبَالِ ٱرْتَعَدَتْ وَٱرْتَجَّتْ لِأَنَّهُ غَضِبَ. ٧ 7
Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi, ndipo maziko a mapiri anagwedezeka; ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
صَعِدَ دُخَانٌ مِنْ أَنْفِهِ، وَنَارٌ مِنْ فَمِهِ أَكَلَتْ. جَمْرٌ ٱشْتَعَلَتْ مِنْهُ. ٨ 8
Mʼmphuno mwake munatuluka utsi; moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake, makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.
طَأْطَأَ ٱلسَّمَاوَاتِ وَنَزَلَ، وَضَبَابٌ تَحْتَ رِجْلَيْهِ. ٩ 9
Iye anangʼamba thambo natsika pansi; pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda.
رَكِبَ عَلَى كَرُوبٍ وَطَارَ، وَهَفَّ عَلَى أَجْنِحَةِ ٱلرِّيَاحِ. ١٠ 10
Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka; nawuluka ndi mphepo mwaliwiro.
جَعَلَ ٱلظُّلْمَةَ سِتْرَهُ. حَوْلَهُ مِظَلَّتَهُ ضَبَابَ ٱلْمِيَاهِ وَظَلَامَ ٱلْغَمَامِ. ١١ 11
Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake, chophimba chake chomuzungulira chinali mitambo yakuda ya mlengalenga.
مِنَ ٱلشُّعَاعِ قُدَّامَهُ عَبَرَتْ سُحُبُهُ. بَرَدٌ وَجَمْرُ نَارٍ. ١٢ 12
Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake munkachokera matalala, makala amoto ndi ziphaliwali zongʼanima.
أَرْعَدَ ٱلرَّبُّ مِنَ ٱلسَّمَاوَاتِ، وَٱلْعَلِيُّ أَعْطَى صَوْتَهُ، بَرَدًا وَجَمْرَ نَارٍ. ١٣ 13
Yehova anabangula kumwamba ngati bingu, mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.
أَرْسَلَ سِهَامَهُ فَشَتَّتَهُمْ، وَبُرُوقًا كَثِيرَةً فَأَزْعَجَهُمْ، ١٤ 14
Iye anaponya mivi yake nabalalitsa adani ake, ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.
فَظَهَرَتْ أَعْمَاقُ ٱلْمِيَاهِ، وَٱنْكَشَفَتْ أُسُسُ ٱلْمَسْكُونَةِ مِنْ زَجْرِكَ يَارَبُّ، مِنْ نَسْمَةِ رِيحِ أَنْفِكَ. ١٥ 15
Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera; maziko a dziko lapansi anakhala poyera, Yehova atabangula mwaukali, pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwanu.
أَرْسَلَ مِنَ ٱلْعُلَى فَأَخَذَنِي. نَشَلَنِي مِنْ مِيَاهٍ كَثِيرَةٍ. ١٦ 16
Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira; anandivuwula mʼmadzi ozama.
أَنْقَذَنِي مِنْ عَدُوِّي ٱلْقَوِيِّ، وَمِنْ مُبْغِضِيَّ لِأَنَّهُمْ أَقْوَى مِنِّي. ١٧ 17
Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, adani anga, amene anali amphamvu kuposa ine.
أَصَابُونِي فِي يَوْمِ بَلِيَّتِي، وَكَانَ ٱلرَّبُّ سَنَدِي. ١٨ 18
Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto, koma Yehova anali thandizo langa.
أَخْرَجَنِي إِلَى ٱلرُّحْبِ. خَلَّصَنِي لِأَنَّهُ سُرَّ بِي. ١٩ 19
Iye anandipititsa kumalo otakasuka; anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.
يُكَافِئُنِي ٱلرَّبُّ حَسَبَ بِرِّي. حَسَبَ طَهَارَةِ يَدَيَّ يَرُدُّ لِي. ٢٠ 20
Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa; molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
لِأَنِّي حَفِظْتُ طُرُقَ ٱلرَّبِّ، وَلَمْ أَعْصِ إِلَهِي. ٢١ 21
Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova; ndilibe mlandu wochoka pamaso Mulungu wanga.
لِأَنَّ جَمِيعَ أَحْكَامِهِ أَمَامِي، وَفَرَائِضَهُ لَمْ أُبْعِدْهَا عَنْ نَفْسِي. ٢٢ 22
Malamulo ake onse ali pamaso panga; sindinasiye malangizo ake.
وَأَكُونُ كَامِلًا مَعَهُ وَأَتَحَفَّظُ مِنْ إِثْمِي. ٢٣ 23
Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
فَيَرُدُّ ٱلرَّبُّ لِي كَبِرِّي، وَكَطَهَارَةِ يَدَيَّ أَمَامَ عَيْنَيْهِ. ٢٤ 24
Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa, molingana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.
مَعَ ٱلرَّحِيمِ تَكُونُ رَحِيمًا. مَعَ ٱلرَّجُلِ ٱلْكَامِلِ تَكُونُ كَامِلًا. ٢٥ 25
Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu; kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
مَعَ ٱلطَّاهِرِ تَكُونُ طَاهِرًا، وَمَعَ ٱلْأَعْوَجِ تَكُونُ مُلْتَوِيًا. ٢٦ 26
kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu, koma kwa achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
لِأَنَّكَ أَنْتَ تُخَلِّصُ ٱلشَّعْبَ ٱلْبَائِسَ، وَٱلْأَعْيُنُ ٱلْمُرْتَفِعَةُ تَضَعُهَا. ٢٧ 27
Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa, koma anthu amtima odzikuza mumawatsitsa.
لِأَنَّكَ أَنْتَ تُضِيءُ سِرَاجِي. ٱلرَّبُّ إِلَهِي يُنِيرُ ظُلْمَتِي. ٢٨ 28
Inu Yehova, sungani nyale yanga kuti iziyakabe; Mulungu wanga wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
لِأَنِّي بِكَ ٱقْتَحَمْتُ جَيْشًا، وَبِإِلَهِي تَسَوَّرْتُ أَسْوَارًا. ٢٩ 29
Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo; ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.
ٱللهُ طَرِيقُهُ كَامِلٌ. قَوْلُ ٱلرَّبِّ نَقِيٌّ. تُرْسٌ هُوَ لِجَمِيعِ ٱلْمُحْتَمِينَ بِهِ. ٣٠ 30
Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro; mawu a Yehova alibe cholakwika. Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa Iye.
لِأَنَّهُ مَنْ هُوَ إِلَهٌ غَيْرُ ٱلرَّبِّ؟ وَمَنْ هُوَ صَخْرَةٌ سِوَى إِلَهِنَا؟ ٣١ 31
Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova? Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?
ٱلْإِلَهُ ٱلَّذِي يُمَنْطِقُنِي بِٱلْقُوَّةِ وَيُصَيِّرُ طَرِيقِي كَامِلًا. ٣٢ 32
Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu ndi kulungamitsa njira yanga.
ٱلَّذِي يَجْعَلُ رِجْلَيَّ كَٱلْإِيَّلِ، وَعَلَى مُرْتَفِعَاتِي يُقِيمُنِي. ٣٣ 33
Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi; Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri.
ٱلَّذِي يُعَلِّمُ يَدَيَّ ٱلْقِتَالَ، فَتُحْنَى بِذِرَاعَيَّ قَوْسٌ مِنْ نُحَاسٍ. ٣٤ 34
Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo; manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo.
وَتَجْعَلُ لِي تُرْسَ خَلَاصِكَ وَيَمِينُكَ تَعْضُدُنِي، وَلُطْفُكَ يُعَظِّمُنِي. ٣٥ 35
Inu mumandipatsa chishango chachipambano, ndipo dzanja lanu lamanja limandichirikiza; mumawerama pansi kundikuza.
تُوَسِّعُ خُطُوَاتِي تَحْتِي، فَلَمْ تَتَقَلْقَلْ عَقِبَايَ. ٣٦ 36
Munakulitsa njira yoyendamo ine, kuti mapazi anga asaguluke.
أَتْبَعُ أَعْدَائِي فَأُدْرِكُهُمْ، وَلَا أَرْجِعُ حَتَّى أُفْنِيَهُمْ. ٣٧ 37
Ndinathamangitsa adani anga ndi kuwapitirira; sindinabwerere mpaka atawonongedwa.
أَسْحَقُهُمْ فَلَا يَسْتَطِيعُونَ ٱلْقِيَامَ. يَسْقُطُونَ تَحْتَ رِجْلَيَّ. ٣٨ 38
Ndinakantha adaniwo kotero kuti sanathenso kudzuka; anagwera pa mapazi anga.
تُمَنْطِقُنِي بِقُوَّةٍ لِلْقِتَالِ. تَصْرَعُ تَحْتِي ٱلْقَائِمِينَ عَلَيَّ. ٣٩ 39
Inu munandiveka ndi mphamvu yokachitira nkhondo, munachititsa kuti ndigonjetse adani anga.
وَتُعْطِينِي أَقْفِيَةَ أَعْدَائِي، وَمُبْغِضِيَّ أُفْنِيهِمْ. ٤٠ 40
Inu munachititsa adani anga kutembenuka, kuonetsa misana yawo pothawa, ndipo ine ndinawononga adani angawo.
يَصْرُخُونَ وَلَا مُخَلِّصَ. إِلَى ٱلرَّبِّ فَلَا يَسْتَجِيبُ لَهُمْ. ٤١ 41
Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa. Analirira kwa Yehova koma sanawayankhe.
فَأَسْحَقُهُمْ كَٱلْغُبَارِ قُدَّامَ ٱلرِّيحِ. مِثْلَ طِينِ ٱلْأَسْوَاقِ أَطْرَحُهُمْ. ٤٢ 42
Ine ndinawaperesa ngati fumbi lowuluka ndi mphepo. Ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.
تُنْقِذُنِي مِنْ مُخَاصَمَاتِ ٱلشَّعْبِ. تَجْعَلُنِي رَأْسًا لِلْأُمَمِ. شَعْبٌ لَمْ أَعْرِفْهُ يَتَعَبَّدُ لِي. ٤٣ 43
Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa anthu; mwandisandutsa kukhala mtsogoleri wa anthu a mitundu ina. Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
مِنْ سَمَاعِ ٱلْأُذُنِ يَسْمَعُونَ لِي. بَنُو ٱلْغُرَبَاءِ يَتَذَلَّلُونَ لِي. ٤٤ 44
Alendo amadzipereka okha pamaso panga; akangomva za ine amandigonjera.
بَنُو ٱلْغُرَبَاءِ يَبْلَوْنَ وَيَزْحَفُونَ مِنْ حُصُونِهِمْ. ٤٥ 45
Iwo onse anataya mtima; anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.
حَيٌّ هُوَ ٱلرَّبُّ، وَمُبَارَكٌ صَخْرَتِي، وَمُرْتَفِعٌ إِلَهُ خَلَاصِي، ٤٦ 46
Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa! Akuzike Mulungu Mpulumutsi wanga!
ٱلْإِلَهُ ٱلْمُنْتَقِمُ لِي، وَٱلَّذِي يُخْضِعُ ٱلشُّعُوبَ تَحْتِي. ٤٧ 47
Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango, amene amagonjetsa anthu a mitundu yonse amene ali pansi pa ulamuliro wanga,
مُنَجِّيَّ مِنْ أَعْدَائِي. رَافِعِي أَيْضًا فَوْقَ ٱلْقَائِمِينَ عَلَيَّ. مِنَ ٱلرَّجُلِ ٱلظَّالِمِ تُنْقِذُنِي. ٤٨ 48
amene amandipulumutsa mʼmanja mwa adani anga. Inu munandikuza kuposa adani anga; munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
لِذَلِكَ أَحْمَدُكَ يَارَبُّ فِي ٱلْأُمَمِ، وَأُرَنِّمُ لِٱسْمِكَ. ٤٩ 49
Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa anthu a mitundu ina, Inu Yehova; ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
بُرْجُ خَلَاصٍ لِمَلِكِهِ، وَٱلصَّانِعُ رَحْمَةً لِمَسِيحِهِ، لِدَاوُدَ وَنَسْلِهِ إِلَى ٱلْأَبَدِ. ٥٠ 50
Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake; amaonetsa chikondi chosasinthika kwa wodzozedwa wake, kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.

< اَلْمَزَامِيرُ 18 >