< حِزْقِيَال 7 >

وَكَانَ إِلَيَّ كَلَامُ ٱلرَّبِّ قَائِلًا: ١ 1
Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti,
«وَأَنْتَ يَا ٱبْنَ آدَمَ، فَهَكَذَا قَالَ ٱلسَّيِّدُ ٱلرَّبُّ لِأَرْضِ إِسْرَائِيلَ: نِهَايَةٌ! قَدْ جَاءَتِ ٱلنِّهَايَةُ عَلَى زَوَايَا ٱلْأَرْضِ ٱلْأَرْبَعِ. ٢ 2
“Iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuwuza dziko la Israeli kuti: “Chimaliziro! Chimaliziro chafika ku ngodya zinayi za dziko.
اَلْآنَ ٱلنِّهَايَةُ عَلَيْكِ، وَأُرْسِلُ غَضَبِي عَلَيْكِ، وَأَحْكُمُ عَلَيْكِ كَطُرُقِكِ، وَأَجْلِبُ عَلَيْكِ كُلَّ رَجَاسَاتِكِ. ٣ 3
Chimaliziro chili pa iwe tsopano. Mkwiyo wanga ndidzawuthira pa iwe. Ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako ndi kukulanga chifukwa cha zonyansa zako.
فَلَا تَشْفُقُ عَلَيْكِ عَيْنِي، وَلَا أَعْفُو، بَلْ أَجْلِبُ عَلَيْكِ طُرُقَكِ وَتَكُونُ رَجَاسَاتُكِ فِي وَسْطِكِ، فَتَعْلَمُونَ أَنِّي أَنَا ٱلرَّبُّ. ٤ 4
Ine sindidzakumvera chisoni kapena kukuleka. Ndidzakulanga ndithu chifukwa cha ntchito zako zoyipa komanso chifukwa cha miyambo yako yonyansa imene ili pakati pako. Pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
«هَكَذَا قَالَ ٱلسَّيِّدُ ٱلرَّبُّ: شَرٌّ! شَرٌّ وَحِيدٌ هُوَذَا قَدْ أَتَى. ٥ 5
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: “Chiwonongeko! Chiwonongeko chimene sichinamvekepo! Taona chikubwera!
نِهَايَةٌ قَدْ جَاءَتْ. جَاءَتِ ٱلنِّهَايَةُ. ٱنْتَبَهَتْ إِلَيْكِ. هَا هِيَ قَدْ جَاءَتْ. ٦ 6
Chimaliziro chafika! Chimaliziro chafika! Chiwonongeko chakugwera. Taona chafika!
ٱنْتَهَى ٱلدَّوْرُ إِلَيْكَ أَيُّهَا ٱلسَّاكِنُ فِي ٱلْأَرْضِ. بَلَغَ ٱلْوَقْتُ. ٱقْتَرَبَ يَوْمُ ٱضْطِرَابٍ، لَا هُتَافُ ٱلْجِبَالِ. ٧ 7
Inu anthu okhala mʼdziko, chiwonongeko chakugwerani. Nthawi yafika, tsiku layandikira; tsiku la chisokonezo osati la chimwemwe pa mapiri.
اَلْآنَ عَنْ قَرِيبٍ أَصُبُّ رِجْزِي عَلَيْكِ، وَأُتَمِّمُ سَخَطِي عَلَيْكِ، وَأَحْكُمُ عَلَيْكِ كَطُرُقِكِ، وَأَجْلِبُ عَلَيْكِ كُلَّ رَجَاسَاتِكِ. ٨ 8
Ine ndili pafupi kukukwiyirani, ndipo ukali wanga udzathera pa iwe; Ine ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako ndiponso ndidzakulanga chifukwa cha miyambo yako yonyansa.
فَلَا تَشْفُقُ عَيْنِي، وَلَا أَعْفُو، بَلْ أَجْلِبُ عَلَيْكِ كَطُرُقِكِ، وَرَجَاسَاتُكِ تَكُونُ فِي وَسْطِكِ، فَتَعْلَمُونَ أَنِّي أَنَا ٱلرَّبُّ ٱلضَّارِبُ. ٩ 9
Ine sindidzakumvera chisoni kapena kukuleka. Ndidzakulanga malingana ndi ntchito zako ndiponso chifukwa cha miyambo yako yonyansa pakati pako.
«هَا هُوَذَا ٱلْيَوْمُ، هَا هُوَذَا قَدْ جَاءَ! دَارَتِ ٱلدَّائِرَةُ. أَزْهَرَتِ ٱلْعَصَا. أَفْرَخَتِ ٱلْكِبْرِيَاءُ. ١٠ 10
“Taona, tsikulo! Taona, lafika! Chiwonongeko chako chabwera. Ndodo yaphuka mphundu za maluwa. Kudzitama kwaphuka.
قَامَ ٱلظُّلْمُ إِلَى عَصَا ٱلشَّرِّ. لَا يَبْقَى مِنْهُمْ وَلَا مِنْ ثَرْوَتِهِمْ وَلَا مِنْ ضَجِيجِهِمْ، وَلَا نَوْحٌ عَلَيْهِمْ. ١١ 11
Chiwawa chasanduka ndodo yowakwapulira chifukwa cha kuyipa kwawo. Palibe mwa anthu amenewo amene adzatsale. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa unyinji wawo. Palibiretu ndipo sipadzapezeka munthu wowalira maliro.
قَدْ جَاءَ ٱلْوَقْتُ. بَلَغَ ٱلْيَوْمُ. فَلَا يَفْرَحَنَّ ٱلشَّارِي، وَلَا يَحْزَنَنَّ ٱلْبَائِعُ، لِأَنَّ ٱلْغَضَبَ عَلَى كُلِّ جُمْهُورِهِمْ. ١٢ 12
Nthawi yafika! Tsiku layandikira! Munthu wogula asakondwere ndipo wogulitsa asamve chisoni, popeza ukali wanga uli pa gulu lonse.
لِأَنَّ ٱلْبَائِعَ لَنْ يَعُودَ إِلَى ٱلْمَبِيعِ، وَإِنْ كَانُوا بَعْدُ بَيْنَ ٱلْأَحْيَاءِ. لِأَنَّ ٱلرُّؤْيَا عَلَى كُلِّ جُمْهُورِهَا فَلَا يَعُودُ، وَٱلْإِنْسَانُ بِإِثْمِهِ لَا يُشَدِّدُ حَيَاتَهُ. ١٣ 13
Wogulitsa sadzazipezanso zinthu zimene anagulitsa kwa wina chinkana onse awiri akanali ndi moyo, pakuti chilango chidzagwera onsewo ndipo sichingasinthike. Chifukwa cha machimo awo, palibe aliyense amene adzapulumutsa moyo wake.
قَدْ نَفَخُوا فِي ٱلْبُوقِ وَأَعَدُّوا ٱلْكُلَّ، وَلَا ذَاهِبَ إِلَى ٱلْقِتَالِ، لِأَنَّ غَضَبِي عَلَى كُلِّ جُمْهُورِهِمْ. ١٤ 14
“Lipenga lalira, ndipo zonse zakonzeka. Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akupita ku nkhondo, pakuti mkwiyo wanga uli pa gulu lonse.
«اَلسَّيْفُ مِنْ خَارِجٍ، وَٱلْوَبَأُ وَٱلْجُوعُ مِنْ دَاخِلٍ. ٱلَّذِي هُوَ فِي ٱلْحَقْلِ يَمُوتُ بِٱلسَّيْفِ، وَٱلَّذِي هُوَ فِي ٱلْمَدِينَةِ يَأْكُلُهُ ٱلْجُوعُ وَٱلْوَبَأُ. ١٥ 15
Ku bwalo kuli kumenyana ndipo mʼkati muli mliri ndi njala. Anthu okhala ku midzi adzafa ndi nkhondo. Iwo okhala ku mizinda adzafa ndi mliri ndi njala.
وَيَنْفَلِتُ مِنْهُمْ مُنْفَلِتُونَ وَيَكُونُونَ عَلَى ٱلْجِبَالِ كَحَمَامِ ٱلْأَوْطِئَةِ. كُلُّهُمْ يَهْدِرُونَ كُلُّ وَاحِدٍ عَلَى إِثْمِهِ. ١٦ 16
Onse amene adzapulumuka ndi kumakakhala ku mapiri, azidzalira ngati nkhunda za ku zigwa. Aliyense azidzabuwula chifukwa cha machimo ake.
كُلُّ ٱلْأَيْدِي تَرْتَخِي، وَكُلُّ ٱلرُّكَبِ تَصِيرُ مَاءً. ١٧ 17
Dzanja lililonse lidzalefuka, ndipo bondo lililonse lidzalobodoka ngati madzi.
وَيَتَنَطَّقُونَ بِٱلْمَسْحِ وَيَغْشَاهُمْ رُعْبٌ، وَعَلَى جَمِيعِ ٱلْوُجُوهِ خِزْيٌ، وَعَلَى جَمِيعِ رُؤُوسِهِمْ قَرَعٌ. ١٨ 18
Iwo adzavala ziguduli ndipo adzagwidwa ndi mantha. Adzakhala ndi nkhope zamanyazi ndipo mitu yawo adzameta mpala.
يُلْقُونَ فِضَّتَهُمْ فِي ٱلشَّوَارِعِ، وَذَهَبُهُمْ يَكُونُ لِنَجَاسَةٍ. لَا تَسْتَطِيعُ فِضَّتُهُمْ وَذَهَبُهُمْ إِنْقَاذَهُمْ فِي يَوْمِ غَضَبِ ٱلرَّبِّ. لَا يُشْبِعُونَ مِنْهُمَا أَنْفُسَهُمْ، وَلَا يَمْلَأُونَ جَوْفَهُمْ، لِأَنَّهُمَا صَارَا مَعْثَرَةَ إِثْمِهِمْ. ١٩ 19
“Iwo adzataya siliva wawo mʼmisewu ndipo golide wawo adzakhala chinthu chonyansa. Siliva ndi golide wawo sizidzatha kuwapulumutsa pa tsiku la ukali wa Yehova. Chuma chawochi sichidzawathandiza kuthetsa njala, kapena kukhala okhuta, pakuti ndicho chinawagwetsa mʼmachimo.
أَمَّا بَهْجَةُ زِينَتِهِ فَجَعَلَهَا لِلْكِبْرِيَاءِ. جَعَلُوا فِيهَا أَصْنَامَ مَكْرُهَاتِهِمْ، رَجَاسَاتِهِمْ، لِأَجْلِ ذَلِكَ جَعَلْتُهَا لَهُمْ نَجَاسَةً. ٢٠ 20
Iwo ankanyadira zodzikongoletsera zawo zamakaka ndipo ankazigwiritsa ntchito kupanga mafano awo onyansa ndi zonyansa zawo zina. Nʼchifukwa chake Ine ndidzazisandutsa kukhala zowanyansa.
أُسْلِمُهَا إِلَى أَيْدِي ٱلْغُرَبَاءِ لِلنَّهْبِ، وَإِلَى أَشْرَارِ ٱلْأَرْضِ سَلْبًا فَيُنَجِّسُونَهَا. ٢١ 21
Ndidzazipereka kwa alendo kuti azifunkhe. Anthu oyipa a dziko lapansi adzazilanda ndi kudziyipitsa.
وَأُحَوِّلُ وَجْهِي عَنْهُمْ فَيُنَجِّسُونَ سِرِّي، وَيَدْخُلُهُ ٱلْمُعْتَنِفُونَ وَيُنَجِّسُونَهُ. ٢٢ 22
Ine ndidzawalekerera anthuwo ndipo adzayipitsa malo anga apamtima. Adzalowamo ngati mbala ndi kuyipitsamo.
«اِصْنَعِ ٱلسِّلْسِلَةَ لِأَنَّ ٱلْأَرْضَ قَدِ ٱمْتَلَأَتْ مِنْ أَحْكَامِ ٱلدَّمِ، وَٱلْمَدِينَةُ ٱمْتَلَأَتْ مِنَ ٱلظُّلْمِ. ٢٣ 23
“Konzani maunyolo, chifukwa dziko ladzaza ndi anthu opha anzawo ndipo mzinda wadzaza ndi chiwawa.
فَآتِي بِأَشَرِّ ٱلْأُمَمِ فَيَرِثُونَ بُيُوتَهُمْ، وَأُبِيدُ كِبْرِيَاءَ ٱلْأَشِدَّاءِ فَتَتَنَجَّسُ مَقَادِسُهُمْ. ٢٤ 24
Ndidzabweretsa mitundu ya anthu oyipitsitsa kuti idzalande nyumba zawo. Ndidzathetsa kunyada kwa anthu amphamvu pamene anthu akunja adzalowa mʼmalo awo achipembedzo ndi kuyipitsamo.
اَلرُّعْبُ آتٍ فَيَطْلُبُونَ ٱلسَّلَامَ وَلَا يَكُونُ. ٢٥ 25
Nkhawa ikadzawafikira adzafunafuna mtendere koma osawupeza.
سَتَأْتِي مُصِيبَةٌ عَلَى مُصِيبَةٍ، وَيَكُونُ خَبَرٌ عَلَى خَبَرٍ، فَيَطْلُبُونَ رُؤْيَا مِنَ ٱلنَّبِيِّ، وَٱلشَّرِيعَةُ تُبَادُ عَنِ ٱلْكَاهِنِ، وَٱلْمَشُورَةُ عَنِ ٱلشُّيُوخِ. ٢٦ 26
Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake, ndipo mphekesera idzatsatana ndi mphekesera inzake. Iwo adzayesa kufuna masomphenya kuchokera kwa mneneri. Adzasowa ansembe owaphunzitsa malamulo, ndipo anthu akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu.
ٱلْمَلِكُ يَنُوحُ وَٱلرَّئِيسُ يَلْبَسُ حَيْرَةً، وَأَيْدِي شَعْبِ ٱلْأَرْضِ تَرْجُفُ. كَطَرِيقِهِمْ أَصْنَعُ بِهِمْ، وَكَأَحْكَامِهِمْ أَحْكُمُ عَلَيْهِمْ، فَيَعْلَمُونَ أَنِّي أَنَا ٱلرَّبُّ». ٢٧ 27
Mfumu idzalira, kalonga adzagwidwa ndi mantha. Manja a anthu a mʼdzikomo azidzangonjenjemera ndi mantha. Ine ndidzawalanga molingana ndi machitidwe awo, ndipo ndidzawaweruza molingana ndi momwe anaweruzira anzawo.

< حِزْقِيَال 7 >